Isaiah 16:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Paja minda ya ku Hesiboni idaguga, yatha pamodzi ndi minda yamphesa ya ku Sibima. Mphesa zake zinkaledzeretsa olamulira anthu a mitundu ina. Kale nthambi zake zinkafika mpaka ku Yazere ndi ku chipululu, ndiponso mpaka kutsidya kwa nyanja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti minda ya ku Hesiboni yalefuka, ndi mpesa wa ku Sibima; ambuye a mitundu athyolathyola mitengo yosankhika yake; iwo anafikira ngakhale ku Yazere, nayendayenda m'chipululu; nthambi zake zinatasa, zinapitirira panyanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Minda ya ku Hesiboni yauma, minda ya mpesa ya ku Sibina yaguga. Atsogoleri a mitundu ina anapondaponda minda ya mpesa wabwino, imene nthambi zake zinakafika ku Yazeri, mpaka kutambalalira ku chipululu. Mizu yake inakafika mpaka ku tsidya la nyanja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti minda ya ku Hesiboni yalefuka, ndi mpesa wa ku Sibimai; ambuye a mitundu atyolatyola mitengo yosankhika yace; iwo anafikira ngakhale ku Yazeri, nayendayenda m'cipululu; nthambi zace zinatasa, zinapitima panyanja.