Isaiah 16:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake ndikulira monga m'mene akulirira anthu a mu mzinda wa Yezere chifukwa cha minda yamphesa ya ku Sibima. Inu anthu a ku Hesiboni ndi Eleale ndikukunyowetsani misozi chifukwa choti mwalephera kupeza zokolola, kaamba ka nkhondo imene yaononga zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake ndidzalira ndi kulira kwa Yazere, chifukwa cha mpesa wa Sibima, ndidzakukhathamiza ndi misozi yanga, iwe Hesiboni ndi Eleyale; chifukwa kuti pa zipatso zako za malimwe, ndi pa masika ako, mfuu wankhondo wagwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kotero Ine ndikulira, monga mmene akulirira anthu a ku Yazeri, chifukwa cha minda ya mpesa ya ku Sibima. Inu anthu a ku Hesiboni, inu anthu a ku Eleali, ndikukunyowetsani ndi misozi! Mwalephera kupeza zokolola, chifukwa cha nkhondo imene inawononga zokolola zonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace ndidzalira ndi kulira kwa Yazeri, cifukwa ca mpesa wa Sibima, ndidzakukhathamiza ndi misozi yanga, iwe Hesiboni ndi Eleale; cifukwa kuti pa zipatso zako za malimwe, ndi pa masika ako, mpfuu wankhondo wagwera.