Isaiah 17:10 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Aisraele, mwaiŵala Mulungu Mpulumutsi wanu, simudamkumbukire Iye amene ndiye thanthwe lokupulumutsani. M'malo mwake, mumabzala mbeu zabwino, kubzalira milungu yachilendo,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa iwe waiwala Mulungu wa chipulumutso chako, sunakumbukira thanthwe la mphamvu zako; chifukwa chake iwe waoka mitengo yokondweretsa, waokapo zipinjiri zachilendo;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu mwayiwalatu Mulungu Mpulumutsi wanu; simunakumbukire Thanthwe, linga lanu. Choncho, ngakhale munadzala mbewu zabwino, ndi kuyitanitsa kunja mitengo ya mpesa,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa iwe waiwala Mulungu wa cipulumutso cako, sunakumbukira thanthwe la mphamvu zako; cifukwa cace iwe waoka mitengo yokondweretsa, waokapo zipinjiri zacilendo;