Isaiah 17:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ankhondo a mitundu ina akubwera ndi mkokomo ngati wa madzi ambiri. Koma Mulungu akuŵadzudzula, ndipo iwo adzathaŵira kutali. Adzapirikitsidwa ngati mankhusu ouluka ndi mphepo pa mapiri, ngati fumbi la kamvulumvulu namondwe asanayambe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mitundu ya anthu idzathamanga ngati kuthamanga kwa madzi ambirimbiri; koma Iye adzawadzudzula, ndipo iwo adzathawira patali, nadzapirikitsidwa monga mankhusu a pamapiri patsogolo pa mphepo, ndi monga fumbi lokwetera patsogolo pa mkuntho wa mphepo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ngakhale ankhondo a mitundu ina akubwera ndi mkokomo ngati wa madzi ambiri, koma adzathawira kutali Mulungu akadzawadzudzula. Yehova adzawapirikitsa ngati mankhusu owuluka ndi mphepo pa phiri, ndi ngati fumbi la kamvuluvulu asanayambe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mitundu ya anthu idzathamanga ngati kuthamanga kwa madzi ambirimbiri; koma Iye adzawadzudzula, ndipo iwo adzathawira patari, nadzapitikitsidwa monga mankhusu a pamapiri patsogolo pa mphepo, ndi monga pfumbi lokwetera patsogolo pa mkunthu wa mphepo.