Isaiah 17:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi yamadzulo ndi oopsa! Koma kusanache, onse azimirira. Umu ndimo m'mene zidzaŵachitire anthu otilanda zathu. Limeneli ndilo tsoka la anthu otibera zinthu zathu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pa nthawi ya madzulo, taonani kuopsa; kusanake, iwo palibe. Ili ndi gawo la iwo amene atifunkha ndi ichi chiwagwera omwe alanda zathu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pofika nthawi yamadzulo zoopsa zidzayamba kuchitika, ndipo zidzakhala zitatha pofika mmawa. Izi ndizo zidzachitikire anthu otilanda zinthu, gawo la amene amatibera zinthu zathu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pa nthawi ya madzulo, taonani kuopsya; kusanace, iwo palibe. Ili ndi gawo la iwo amene atifunkha ndi ici ciwagwera omwe alanda zathu.