Isaiah 17:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ku Efuremu sikudzakhalanso linga, ndipo ku Damasiko sikudzakhalanso ufumu. Otsalira a ku Siriya adzachotsedwa ulemu monga anthu a ku Israele,” akutero Chauta Wamphamvuzonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ku Efuremu sikudzakhalanso linga, ngakhale ufumu ku Damasiko, ngakhale otsala kwa Aramu; iwo adzakhala ngati ulemerero wa ana a Israele, ati Yehova wa makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ku Efereimu sikudzakhalanso linga, ndipo ku Damasiko sikudzakhalanso ufumu; Otsalira a ku Siriya adzachotsedwa ulemu monga anthu a ku Israeli,” akutero Yehova Wamphamvuzonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ku Efraimu sikudzakhalanso linga, ngakhale ufumu ku Damasiko, ngakhale otsala kwa Aramu; iwo adzakhala ngati ulemerero wa ana a Israyeli, ati Yehova wamakamu.