Isaiah 17:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Israele adzakhala ngati munda watirigu umene adatsiriza kukolola. Adzakhalanso ngati munda wa m'chigwa cha Refaimu, anthu atatha kukunkha ngala za tirigu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo padzakhala ngati wamasika alikumweta tirigu wosacheka, ndi dzanja lake lilikudula ngala; inde padzakhala ngati pamene wina akunkha ngala m'chigwa cha Refaimu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Israeli adzakhala ngati munda wa tirigu umene anatsiriza kukolola. Adzakhalanso ngati munda wa mʼchigwa cha Refaimu anthu atatha kukunkha ngala za tirigu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo padzakhala ngati wamasika alikumweta tirigu wosaceka, ndi dzanja lace lirikudula ngala; inde padzakhala ngati pamene wina akunkha ngala m'cigwa ca Refaimu.