Isaiah 17:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ochepa okha adzatsalako, monga pogwedeza mtengo wa olivi, zimatsalako ndithu zipatso ziŵiri kapena zitatu pa nthambi ya pamwamba penipeni, kapenanso zinai kapena zisanu pa nthambi zam'munsi,” akutero Chauta, Mulungu wa Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma mudzasiyidwa m'menemo khunkha, monga ngati kugwedeza kwake kwa mtengo wa azitona, zipatso ziwiri pena zitatu m'nsonga ya nthambi yosomphoka, zinai pena zisanu m'nthambi za kunthemba, za mtengo wobalitsa, ati Yehova, Mulungu wa Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Komabe Aisraeli ochepa okha ndiwo ati adzatsale monga mʼmene zimatsalira zipatso ziwiri kapena zitatu pa nthambi ya pamwamba penipeni kapena zipatso zisanu pa nthambi za mʼmunsi mwa mtengo wa olivi akawugwedeza,” akutero Yehova, Mulungu wa Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma mudzasiyidwa m'menemo khunkha, monga ngati kugwedeza kwace kwa mtengo waazitona, zipatso ziwiri pena zitatu m'nsonga ya nthambi yosomphoka, zinai pena zisanu m'nthambi za kunthemba, za mtengo wobalitsa, ati Yehova, Mulungu wa Israyeli.