Isaiah 17:8 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Sadzakhulupiriranso maguwa amene iwo omwe adamanga, kapenanso kudalira zimene adapanga ndi manja ao, ngakhale mafano ofanizira Asera kapena maguwa ofukizapo lubani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo iye sadzayang'ana pa maguwa a nsembe, ntchito ya manja ake, ngakhale kulemekeza chimene anachipanga ndi zala zake, ngakhale zifanizo pena mafano a dzuwa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwo sadzakhulupiriranso maguwa ansembe, ntchito ya manja awo, ndipo sadzadaliranso mitengo ya mafano a Asera, ndiponso maguwa ofukizirapo lubani amene manja awo anapanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo iye sadzayang'ana pa maguwa a nsembe, nchito ya manja ace, ngakhale kulemekeza cimene anacipanga ndi zala zace, ngakhale zifanizo pena mafano a dzuwa.