Isaiah 17:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo mizinda yamphamvu ya Aisraele idzasiyidwa monga mizinda ya Aamori ndi ya Ahivi imene anthu adaaisiya pothaŵa Aisraelewo. Ndipo idzakhala mabwinja.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku limenelo midzi yake yolimba idzakhala ngati mabwinja a m'nkhalango, ndi a pansonga pa phiri, osiyidwa pamaso pa ana a Israele; ndipo padzakhala bwinja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo mizinda yawo yamphamvu, imene anasiya chifukwa cha Aisraeli, idzakhala ngati malo osiyidwa kuti awirire ndi kumera ziyangoyango. Ndipo yonse idzakhala mabwinja.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku limenelo midzi yace yolimba idzakhala ngati mabwinja a m'nkhalango, ndi a pansonga pa phiri, osiyidwa pamaso pa ana a Israyeli; ndipo padzakhala bwinja.