Isaiah 18:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kuchokera ku dzikolo amatuma akazembe pa mtsinje wa Nailo m'mabwato agumbwa omangoyandama pa madzi. Tsono pitani inu amithenga aliŵiro kwa mtundu wa anthu ataliatali ndi a khungu losalala, oopedwa ndi anthu akufupi ndi akutali omwe, mtundu wamphamvu ndi wogonjetsa mitundu ina, anthu amene dziko lao nlodukanadukana ndi mitsinje.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
limene litumiza mithenga panyanja m'ngalawa zamagumbwa zoyenda m'madzi, ndi kuti, Mukani, inu mithenga yoyenda msangamsanga kumtundu wa anthu aatali ndi osalala, kwa mtundu woopsa chikhalire chao, mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lake nyanja ziligawa!
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Dziko limenelo limatumiza akazembe pa mtsinje wa Nailo, mʼmabwato amabango amene amayandama pa madzi, ndikunena kuti, “Pitani, inu amithenga aliwiro, kwa mtundu wa anthu ataliatali a khungu losalala, ndi woopedwa ndi anthu. Akazembe anatumidwa ku dziko la anthu amphamvu ndi logonjetsa anthu ena. Dziko lawo ndi logawikanagawikana ndi mitsinje.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
limene litumiza mithenga panyanja m'ngalawa zatnabungwa zoyenda m'madzi, ndi kuti, Mukani, inu mithenga yoyenda msanga msanga ku mtundu wa anthu atari ndi osalala, kwa mtundu woopsya cikhalire cao, mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lace nyanja ziligawa!