Isaiah 18:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu nonse anthu a pa dziko lapansi, inu amene mumakhala pansi pano, pamene mbendera yakwezedwa pa mapiri, muyang'ane! Lipenga likamalira, mumve!
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Inu nonse akukhala m'dziko lapansi, ndi inu akukhazikika pa dziko lapansi, potukulidwa chizindikiro pamwamba pa mapiri, mudzaona, ndi polizidwa lipenga mudzamva.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu nonse anthu a pa dziko lonse, inu amene mumakhala pa dziko lapansi, pamene mbendera yakwezedwa pa mapiri yangʼanani, ndipo pamene lipenga lilira mumvere.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Inunonseakukhala m'dziko lapansi, ndi inu akukhazikika pa dziko lapansi, potukulidwa cizindikiro pamwamba pa mapiri, mudzaona, ndi polizidwa lipenga mudzamva.