Isaiah 18:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu asanayambe kukolola, maluŵa atayoyoka ndipo mphesa zitayamba kupsa, Iye adzadula mphukira ndi chigwandali, ndipo adzasadza nthambi zotambalala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti masika asanafike, kutatha kuphuka ndi posanduka duwa mphesa yofuna kutcha, iye adzadzombolera tinthambi ndi chikwakwa, ndi nthambi zotasa adzazichotsa ndi kuzisadza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pakuti, anthu asanayambe kukolola, maluwa atayoyoka ndiponso mphesa zitayamba kupsa, Iye adzadula mphukira ndi mipeni yosadzira, ndipo adzadula ndi kuchotsa nthambi zotambalala.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti masika asanafike, kutatha kuphuka ndi posanduka duwa mphesa yofuna kucha, iye adzadzombolera tinthambi ndi mphopo, ndi nthambi zotasa adzazicotsa ndi kuzisadza.