Isaiah 18:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mitembo ya ankhondowo adzasiyira mbalame zam'mapiri zodya nyama, ndiponso zilombo zakuthengo. Mbalame zidzaidya pa nthaŵi ya chilimwe, ndipo zilombo zakuthengo zidzaidya pa nthaŵi ya chisanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Adzasiyira mbalame zakulusa za m'mapiri ndi zilombo za dziko nthambizo, ndipo mbalame zakulusa zidzakhalapo m'dzinja, ndi zilombo zonse za dziko zidzakhalapo m'malimwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mitembo ya anthu ankhondo adzasiyira mbalame zamʼmapiri zodya nyama ndiponso zirombo zakuthengo; mbalame zidzadya mitemboyo nthawi yonse ya chilimwe, ndipo zirombo zidzayidya pa nthawi yonse yachisanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Adzasiyira mbalame zakulusa za m'mapiri ndi zirombo za dziko nthambizo, ndipo mbalame zakulusa zidzakhalapo m'dzinja, ndi zirombo zonse za dziko zidzakhalapo m'malimwe.