Isaiah 18:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa nthaŵi imeneyo anthu adzabwera ndi zopereka kwa Chauta Wamphamvuzonse. Anthu ake adzakhala aatali ndi a khungu losalala, oopedwa ndi anthu akufupi ndi akutali omwe, mtundu wamphamvu ndi wogonjetsa mitundu ina, anthu amene dziko lao ndi lodukanadukana ndi mitsinje. Zoperekazo adzabwera nazo ku phiri la Ziyoni kumene anthu amapembedza Chauta Wamphamvuzonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nthawi imeneyo mphatso idzaperekedwa kwa Yehova wa makamu, mtundu wa anthu aatali ndi osalala, yochokera kwa mtundu woopsa chikhalire chao; mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lake nyanja ziligawa, kumalo a dzina la Yehova wa makamu, phiri la Ziyoni.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa nthawi imeneyo anthu adzabwera ndi mphatso kwa Yehova Wamphamvuzonse, zochokera kwa anthu ataliatali ndi osalala, kuchokera kwa mtundu wa anthu woopedwa ndi anthu apafupi ndi akutali omwe, mtundu wa anthu amphamvu ndi a chiyankhulo chachilendo, anthu amene dziko lawo ndi logawikanagawikana ndi mitsinje. Adzabwera nazo mphatso ku Phiri la Ziyoni, ku malo a Dzina la Yehova Wamphamvuzonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nthawi imeneyo mphatso idzaperekedwa kwa Yehova wa makamu, mtundu wa anthu atari ndi osalala, yocokera kwa mtundu woopsya cikhalire cao; mtundu umene uyesa dziko ndi kupondereza pansi, umene dziko lace nyanja ziligawa, ku malo a dzina la Yehova wa makamu, phiri la Ziyoni.