Isaiah 19:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nawu ulosi wonena za Ejipito. Chauta wakwera pa mtambo wothamanga, akupita ku Ejipito. Mafano a ku Ejipito adzanjenjemera pamaso pake, ndipo Aejipitowo mitima yao idzachokamo ndi mantha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Katundu wa Ejipito. Taonani, Yehova wakwera pamwamba pa mtambo wothamanga, nadza ku Ejipito; ndi mafano a Ejipito adzagwedezeka pakufika kwake, ndi mtima wa Ejipito udzasungunuka pakati pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uthenga onena za Igupto: Taonani, Yehova wakwera pa mtambo waliwiro, ndipo akupita ku Igupto. Mafano a ku Igupto akunjenjemera pamaso pake, ndipo mitima ya Aigupto yachokamo ndi mantha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Katundu wa Aigupto. Taonani, Yehova wakwera pamwamba pa mtambo wothamanga, nadza ku Aigupto; ndi mafano a Aigupto adzagwedezeka pakufika kwace, ndi mtima wa Aigupto udzasungunuka pakati pace.