Isaiah 19:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwe Farao, anzeru ako ali kuti? Abwere kuno msanga kuti akudziŵitse zimene Chauta Wamphamvuzonse akunena zotsutsa Ejipito.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nanga tsopano anzeru ali kuti? Akuuze iwe tsopano; adziwe chimene Yehova wa makamu watsimikiza mtima kuchitira Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iwe Farao, anthu ako anzeru ali kuti? Abweretu kuti akuwuze ndi kukudziwitsa zimene Yehova Wamphamvuzonse wakonza kuchitira dziko la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nanga tsopano anzeru ali kuti? akuuze iwe tsopano; adziwe cimene Yehova wa makamu watsimikiza mtima kucitira Aigupto.