Isaiah 19:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akalonga a mu mzinda wa Zowani asanduka zitsilu, ndipo akalonga a ku Memfisi anyengedwa. Amene ali atsogoleri a Aejipito alisokeza dziko lao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Akalonga a Zowani apusa, akalonga a Nofi anyengedwa; iwo asocheretsa Ejipito, amene ali mwala wa pangodya wa mafuko ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Akuluakulu a ku Zowani asanduka zitsiru, atsogoleri a ku Mefisi anamizidwa; atsogoleri a dziko la Igupto asocheretsa anthu a dzikolo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Akalonga a Zoani apusa, akalonga a Nofi anyengedwa; iwo asoceretsa Aigupto, amene ali mwala wa pangondya wa mapfuko ace.