Isaiah 19:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta waŵasokoneza Aejipito. Iwo akuchita dzandidzandi pa ntchito zao zonse, ngati chidakwa choterereka pa masanzi ake omwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Yehova wasanganiza mzimu wa kusaweruzika pakati pake; ndipo iwo asocheretsa Ejipito m'ntchito zake zonse, monga mwamuna woledzera ayenda punzipunzi posanza pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova wasocheretsa anthu a ku Igupto. Iwo akuchita kudzandira pa zonse zimene akuchita, ngati chidakwa choterereka pa masanzi ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Yehova wasanganiza mzimu wa kusaweruzika pakati pace; ndipo iwo asoceretsa Aigupto m'nchito zonse zace, monga mwamuna woledzera ayenda punzipunzi posanza pace.