Isaiah 19:16 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo Aejipito adzakhala ngati akazi, adzanjenjemera ndi kuchita mantha, akadzaona Chauta Wamphamvuzonse akusamula dzanja kufuna kuŵalanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku limenelo Ejipito adzanga akazi; ndipo adzanthunthumira ndi kuopa, chifukwa cha kugwedeza kwa dzanja la Yehova wa makamu, limene Iye agwedeza pamwamba pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo Aigupto adzakhala ngati amayi. Adzanjenjemera ndi kuchita mantha akadzaona Yehova Wamphamvuzonse, atakweza dzanja lake kufuna kuwalanga.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku limenelo Aigupto adzanga akazi; ndipo adzanthunthumira ndi kuopa, cifukwa ca kugwedeza kwa dzanja la Yehova wa makamu, limene Iye agwedeza pamwamba pace.