Isaiah 19:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko la Yuda lidzaopsa dziko la Ejipito. Ndipo nthaŵi zonse Aejipito akadzamva za Yuda, adzaopsedwa chifukwa cha zimene Chauta Wamphamvuzonse afuna kuŵachita Aejipitowo kudzera mwa Yudayo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo dziko la Yuda lidzaopsa Ejipito, yense wakulitchula adzamtembenukira mwamantha, chifukwa cha uphungu wa Yehova wa makamu, aupanga pa dzikolo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ndipo dziko la Yuda lidzaopsa dziko la Aigupto. Aliyense amene adzamve dzina la Yuda adzaopsedwa chifukwa cha zimene Yehova Wamphamvuzonse wakonzekera kuchitira dziko la Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo dziko la Yuda lidzaopsa Aigupto, yense wakulichula adzamtembenukira mwamantha, cifukwa ca uphungu wa Yehova wa makamu, aupanga pa dzikolo.