Isaiah 19:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo ku dziko la Ejipito kudzakhala mizinda isanu yolankhula Chihebri, ndipo anthu ake adzalumbira kwa Chauta Wamphamvuzonse kuti adzamtumikira. Umodzi mwa mizindayo udzatchulidwa “Mzinda wa Dzuŵa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku limenelo padzakhala midzi isanu m'dziko la Ejipito yolankhula chinenero cha Kanani, ndi yolumbira, Pali Yehova wa makamu; wina udzatchedwa, Mudzi wa chionongeko.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo ku dziko la Igupto kudzakhala mizinda isanu yoyankhula chiyankhulo cha Akanaani, ndipo anthu ake adzalumbira kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti adzamutumikira. Umodzi mwa mizindayo udzatchedwa Mzinda Wachilungamo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku limenelo padzakhala midzi isanu m'dziko la Aigupto yolankhula cinenero ca Kanani, ndi yolumbira, Pali Yehova wa makamu; wina udzachedwa, Mudzi wa cionongeko.