Isaiah 19:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono Ine ndidzautsa Aejipito kuti amenyane okhaokha. Ndipo adzamenyana, mbale ndi mbale wake, mnansi ndi mnansi wake, mzinda ndi mzinda unzake, ndiponso ufumu ndi ufumu unzake.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo ndidzapikisanitsa Aejipito; ndipo adzamenyana wina ndi mbale wake, ndi wina ndi mnansi wake; mudzi kumenyana ndi mudzi, ndi ufumu kumenyana ndi ufumu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ine ndidzadzutsa Aigupto kuti amenyane okhaokha; mʼbale adzamenyana ndi mʼbale wake, mnansi ndi mnansi wake, mzinda ndi mzinda unzake, ndiponso ufumu ndi ufumu unzake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo ndidzapikisanitsa Aaigupto; ndipo adzamenyana wina ndi mbale wace, ndi wina ndi mnansi wace; mudzi kumenyana ndi mudzi, ndi ufumu kumenyana ndi ufumu.