Isaiah 19:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimenezo zidzakhala umboni wozindikiritsa kuti Chauta Wamphamvuzonse alimo m'dziko la Ejipito. Aejipito akadzalira kwa Chauta pa zovuta zao, Iye adzatuma mpulumutsi kuti aŵateteze ndi kuŵapulumutsa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo chidzakhala chizindikiro ndi mboni ya Yehova wa makamu m'dziko la Ejipito; pakuti iwo adzalirira kwa Yehova, chifukwa cha osautsa, ndipo Iye adzawatumizira mpulumutsi, ndi wamphamvu, nadzawapulumutsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zimenezo zidzakhala umboni wozindikiritsa kuti Yehova Wamphamvuzonse alimo mʼdziko la Igupto. Pamene Aigupto adzalirira Yehova chifukwa cha owapondereza, Iye adzawatumizira mpulumutsi ndi mtetezi ndipo adzawalanditsa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo cidzakhala cizindikiro ndi mboni ya Yehova wa makamu m'dziko la Aigupto; pakuti iwo adzalirira kwa Yehova, cifukwa ca osautsa, ndipo Iye adzawatumizira mpulumutsi, ndi wamphamvu, nadzawapulumutsa.