Isaiah 19:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidzalepheretsa zolinga za Aejipito mwakuti adzataya mtima. Tsono adzapempha nzeru kwa mafano, amaula, olankhula ndi mizimu, ndiponso anyanga.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mzimu wa Ejipito adzakhala wachabe pakati pake; ndipo Ine ndidzaononga uphungu wake; ndimo iwo adzafunafuna mafano ndi anyanga, ndi alauli, ndi obwebweta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Aigupto adzataya mtima popeza ndidzalepheretsa zolinga zawo; adzapempha nzeru kwa mafano awo ndiponso kwa woyankhula ndi mizimu ya anthu akufa, kwa amawula ndi kwa oyankhula ndi mizimu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mzimu wa Aigupto adzakhala wacabe pakati pace; ndipo Ine ndidzaononga uphungu wace; ndimo iwo adzafunafuna mafano ndi anyanga, ndi alauli, ndi obwebweta.