Isaiah 2:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo anthu adzatayira mfuko ndi mileme mafano asiliva ndi agolide, amene adaadzipangira kuti azipembedza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku limenelo munthu adzataya kumfuko ndi kumileme mafano ake asiliva ndi agolide amene anthu anampangira iye awapembedze;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo anthu adzatayira mfuko ndi mileme mafano awo asiliva ndi mafano awo agolide, amene anawapanga kuti aziwapembedza.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku limenelo munthu adzataya ku mfuko ndi ku mileme mafano ace asiliva ndi agolidi amene anthu anampangira iye awapembedze;