Isaiah 2:21 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzathaŵira m'mapanga am'matanthwe ndi m'ming'alu yam'nthaka, kuthaŵa mkwiyo wa Chauta, kuthaŵanso ulemerero wa ufumu wake, pamene Iye adzabwere kudzaopsa dziko lapansi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
kuti akalowe m'mapanga a m'matanthwe, ndi m'mindala a m'miyala, kuthawa kuopsa kwa Yehova, ndi ulemerero wachifumu wake, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Adzathawira mʼmapanga a matanthwe ndiponso mʼmingʼalu ya nthaka kuthawa mkwiyo wa Yehova ndiponso ulemerero wa ufumu wake, pamene Iye adzuka kugwedeza dziko lapansi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
kuti akalowe m'mapanga a m'matanthwe, ndi m'mindala a m'miyala, kuthawa kuopsya kwa Yehova, ndi ulemerero wacifumu wace, podzuka Iye kugwedeza dziko ndi mphamvu,