Isaiah 2:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Anthu a mitundu yambiri adzabwera, ndipo adzanena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Chauta, ku Nyumba ya Mulungu wa Yakobe. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda m'njira zakezo.” Pakutitu nku Ziyoni kumene kudzafumira malangizo akewo, nku Yerusalemu kumene kudzachokera mau a Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka kuphiri la Yehova, kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zake, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ake; chifukwa m'Ziyoni mudzatuluka chilamulo, ndi mau a Yehova kuchokera m'Yerusalemu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Anthu ambiri adzabwera ndikunena kuti, “Tiyeni tikwere ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo. Iye adzatiphunzitsa njira zake, ndipo tidzayenda mʼnjira zakezo.” Malangizo adzachokera ku Ziyoni, mawu a Yehova adzachokera ku Yerusalemu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anthu ambiri adzanka, nati, Tiyeni tikwere kunka ku phiri la Yehova, ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo; ndipo Iye adzatiphunzitsa za njira zace, ndipo tidzayenda m'mayendedwe ace; cifukwa m'Ziyoni mudzaturuka cilamulo, ndi mau a Yehova kucokera m'Yerusalemu.