Isaiah 2:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iyeyo adzaweruza pakati pa mitundu ya anthu, adzathetsa kusamvana pakati pa mafuko ambiri. Anthuwo adzasula malupanga ao kuti akhale makasu, ndiponso mikondo yao kuti ikhale mapwitika. Mitundu ya anthu sidzasamulirananso malupanga, sidzaphunziranso zomenyana nkhondo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale zolimira, ndi nthungo zao zikhale makasu; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye adzaweruza pakati pa mayiko, ndipo adzathetsa kusamvana pakati pa anthu ambiri. Anthuwo adzasandutsa malupanga awo kukhala makasu ndiponso mikondo yawo kukhala zomwetera. Mtundu wina sudzatenganso lupanga kumenyana ndi mtundu wina, kapena kuphunziranso za nkhondo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye adzaweruza pakati pa akunja, adzadzudzula mitundu yambiri ya anthu; ndipo iwo adzasula malupanga ao akhale zolimira, ndi nthungo zao zikhale anangwape; mtundu sudzanyamula lupanga kumenyana ndi mtundu wina, ndipo sadzaphunziranso nkhondo.