Isaiah 2:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Inu Mulungu, mwakana anthu anu, zidzukulu za Yakobe. Dziko ladzaza ndi anthu amatsenga akuvuma, ladzazanso ndi olosa a ku Filistiya. Anthu anu akuchita nao miyambo yachilendo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa inu mwasiya anthu anu a nyumba ya Yakobo, chifukwa kuti iwo adzazidwa ndi miyambo ya kum'mawa, ndipo ali olaula ngati Afilisti, naomba m'manja ndi ana a achilendo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Inu Yehova mwawakana anthu anu, nyumba ya Yakobo. Iwo adzaza ndi zamatsenga zochokera Kummawa; amawombeza mawula ngati Afilisti, ndipo amayanjana ndi anthu osapembedza Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa inu mwasiya anthu anu a nyumba ya Yakobo, cifukwa kuti iwo adzazidwa ndi miyambo ya kum'mawa, ndipo ali olaula ngati Afilisti, naomba m'manja ndi ana a acilendo.