Isaiah 20:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi imeneyo nkuti Chauta atalankhula kale kudzera mwa Yesaya mwana wa Amozi. Adaanena kuti, “Pita ukavule chiguduli m'chiwuno mwako ndi nsapato kuphazi kwako.” Ndipo iyeyo adaachitadi zimenezo. Ankangoyenda maliseche ndiponso opanda nsapato.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Nthawi imeneyo Yehova ananena ndi Yesaya, mwana wa Amozi, nati, Muka numasule chiguduli m'chuuno mwako, nuchichotse, nuvule nsapato yako kuphazi lako. Ndipo iye anatero, nayenda maliseche, ndi wopanda nsapato.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
nthawi imeneyo Yehova anawuza Yesaya mwana wa Amozi kuti, “Pita kavule chiguduli ndi nsapato zako.” Ndipo iye anaterodi, ankangoyenda wamaliseche ndiponso wopanda nsapato.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Nthawi imeneyo Yehova ananena ndi Yesaya, mwana wa Amozi, nati, Muka numasule ciguduli m'cuuno mwako, nucicotse, nubvule nsapato yako ku phazi lako. Ndipo iye anatero, nayenda marisece, ndi wopanda nsapato,