Isaiah 20:3 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono mzinda wa Asidodi uja utalandidwa, Chauta adati, “Yesaya mtumiki wanga wakhala akuyenda maliseche ndiponso opanda nsapato zaka zitatu zapitazi. Chimenechi chakhala chizindikiro kwa Aejipito ndi Aetiopiya cholosera zimene zilikudza.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova anati, Monga mtumiki wanga Yesaya wayenda maliseche ndi wopanda nsapato zaka zitatu, akhale chizindikiro ndi chodabwitsa kwa Ejipito ndi kwa Etiopiya;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kenaka Yehova anati, “Monga momwe mtumiki wanga Yesaya wakhala akuyendera wamaliseche ndiponso wopanda nsapato kwa zaka zitatu ngati chizindikiro ndi chenjezo kwa dziko la Igupto ndi Kusi,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova anati, Monga mtumiki wanga Yesaya wayenda marisece ndi wopanda nsapato zaka zitatu, akhale cizindikilo ndi codabwitsa kwa Aigupto ndi kwa Etiopia;