Isaiah 20:4 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndimo m'mene mfumu ya ku Asiriya idzachitire: idzatenga akapolo a ku Ejipito ndi opirikitsidwa ku Etiopiya, anyamata ndi okalamba, nidzaŵayendetsa ali maliseche ndi opanda nsapato, matako ao ali pamtunda. Zimenezi zidzachititsa manyazi Aejipitowo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
momwemo mfumu ya Asiriya idzatsogolera kwina am'nsinga a Ejipito, ndi opirikitsidwa a Etiopiya, ana ndi okalamba, amaliseche ndi opanda nsapato, ndi matako osavala, kuti achititse manyazi Ejipito.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
momwemonso mfumu ya ku Asiriya idzatenga ukapolo anthu a ku Igupto ndi a ku Kusi, anyamata ndi okalamba. Iwo adzakhala amaliseche ndi opanda nsapato, matako ali pa mtunda. Zimenezi zidzachititsa manyazi Igupto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
momwemo mfumu ya Asuri idzatsogolera kwina am'nsinga a Aigupto, ndi opitikitsidwa a Etiopia, ana ndi okalamba, amarisece ndi opanda nsapato, ndi matako osabvala, kuti acititse manyazi Aigupto.