Isaiah 20:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo anthu okhala m'mphepete mwa nyanja adzati, ‘Onanitu zimene zachitikira anthu aja tinkaŵakhulupiriraŵa, amene tinkathaŵirako kuti atithandize ndi kutipulumutsa kwa mfumu ya ku Asiriya! Ha! Tsopano tonsefe tidzapulumuka bwanji?’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wokhala m'mphepete mwa nyanja muno adzati tsiku limenelo, Taonani, kuyembekeza kwathu kuli kotero, kumene ife tinathawira atithangate kupulumutsidwa kwa mfumu ya Asiriya, ndipo ife tidzapulumuka bwanji?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Tsiku limenelo anthu amene amakhala mʼmbali mwa nyanja adzati, ‘Taonani zomwe zawachitikira amene ife tinkawadalira, amene ife tinkathawirako kuti atithandize ndi kutipulumutsa kwa mfumu ya ku Asiriya! Nanga ife tidzapulumuka bwanji?’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wokhala m'mphepete mwa nyanja muno adzati tsiku limenelo, Taonani, kuyembekeza kwathu kuli kotero, kumene ife tinathawira atithangate kupulumutsidwa kwa mfumu ya Asuri, ndipo ife tidzapulumuka bwanji?