Isaiah 21:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nawu ulosi wonena za chipululu cha m'mbali mwa nyanja. Tsoka lidzafika kuchokera ku dziko lochititsa mantha monga m'mene kamvulumvulu amakunthira kuchokera ku chipululu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Katundu wa chipululu cha kunyanja. Monga akamvulumvulu a kumwera apitirira, kufumira kuchipululu kudziko loopsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uthenga wonena za chipululu cha mʼmbali mwa Nyanja. Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya adzabwera ngati kamvuluvulu amene akuwomba modutsa mʼmbali ya nyanja, kuchokera ku chipululu, dziko lochititsa mantha.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Katundu wa cipululu ca kunyanja. Monga akabvumvulu a kumwela apitirira, kufumira kucipululu ku dziko loopsya.