Isaiah 21:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nawu ulosi wonena za Edomu: Wina akundilankhula mofuula kuchokera ku Edomu, akuti, “Iwe mlonda, usikuwu utha liti? Iwe mlonda, utha liti kodi usikuwu?”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Katundu wa Duma. Wina aitana kwa ine kuchokera ku Seiri, Mlonda, nthawi yanji ya usiku? Mlonda, nthawi yanji ya usiku?
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uthenga wonena za Duma: Munthu wina akundiyitana kuchokera ku Seiri kuti, “Iwe mlonda, usikuwu utha liti? Iwe mlonda, utha liti kodi usikuwu?”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Katundu wa Duma. Wina aitana kwa ine kucokera ku Seiri, Mlonda, nthawi yanji ya usiku? Mlonda, nthawi yanji ya usiku?