Isaiah 21:2 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndaona zinthu zoopsa m'masomphenya: wofunkha akufunkha, woononga akuwononga. Ankhondo a ku Elamu, yambani nkhondo! Ankhondo a ku Mediya, zingani mzindawo. Ine Chauta ndidzathetsa mavuto onse amene adadza ndi Babiloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Masomphenya ovuta aonetsedwa kwa ine; wogula malonda wonyenga amangonyenga, ndi wofunkha amangofunkha. Kwera Elamu iwe; zunguniza Mediya iwe; kuusa moyo kwake konse ndakutonthoza.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ine ndaona zinthu zoopsa mʼmasomphenya: Wonyenga akunyenga, wofunkha akufunkha komanso owononga akuwononga. Elamu, yambani nkhondo! Mediya, zingani mzinda! Ine ndidzathetsa mavuto onse amene anayambitsa Ababuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Masomphenya obvuta aonetsedwa kwa ine; wogula malonda wonyenga amangonyenga, ndi wofunkha amangofunkha. Kwera Elamu iwe; zunguniza Media iwe; kuusa moyo kwace konse ndakutonthoza.