Isaiah 21:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake zimene ndidazimva ndi kuziwona m'masomphenya zija zandichititsa mantha, ndipo ndamva nazo ululu ngati mkazi amene akuchira. Ndikuvutika nazo zimene ndilikumva. Ndikuda nazo nkhaŵa zimene ndikuwonazi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chifukwa chake m'chuuno mwanga mwadzazidwa ndi zopota; zopweteka zandigwira ine monga zopweteka za mkazi pobala mwana; zowawa zindiweramitsa, makutu anga sangathe kumva; ndichita mantha sindingathe kuona.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chifukwa cha zimenezi thupi langa likunjenjemera ndi mantha, ndikumva ululu ngati wa mayi amene akubereka; ndikuvutika kwambiri ndi zimene ndikumva, ndathedwa nzeru ndi zimene ndikuziona.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cifukwa cace m'cuuno mwanga mwadzazidwa ndi zopota; zopweteka zandigwira ine monga zopweteka za mkazi pobala mwana; zowawa zindiweramitsa, makutu anga sangathe kumva; ndicita mantha sindingathe kuona.