Isaiah 21:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Iwo akukonza tebulo ndi kuyala mphasa, alikudya, alikumwa. Mwadzidzidzi alikumva mau akuti, Dzukani inu ankhondo, pakani mafuta zishango zanu!
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iwo akonza pa gome lodyera, aika alonda, adya, namwa; ukani, akalonga inu, dzozani mafuta chikopa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ankhondo a ku Elamu ndi Mediya akukonza matebulo, akuyala mphasa, akudya komanso kumwa! Mwadzidzidzi anamva mawu akuti, “Dzukani inu ankhondo, pakani mafuta zishango zanu!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iwo akonza pa gome lodyera, aika alonda, adya, namwa; ukani, akalonga inu, dzozani mafuta cikopa.