Isaiah 21:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Akamaona anthu aŵiriaŵiri okwera pa akavalo, okwera pa abulu ndi okwera pa ngamira, mlondayo akhale tcheru, tcherutu zedi!”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo pamene iye anaona khamu, amuna apakavalo awiriawiri, khamu la abulu, khamu la ngamira, iye adzamvetsera ndi khama mosamalitsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, anthu akubwera ali pa akavalo ndipo akuyenda awiriawiri, okwera pa bulu kapena okwera pa ngamira, mlondayo akhale tcheru kwambiri.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo pamene iye anaona khamu, amuna apakavalo awiri awiri, khamu la aburu, khamu la ngamila, iye adzamvetsera ndi khama mosamalitsa.