Isaiah 21:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndidangoona kukubwera anthu okwera pa akavalo, akuyenda aŵiriaŵiri. Mmodzi mwa iwo adati, ‘Ii, wagwa, wagwatu uku Babiloni! Mafano onse a milungu yake aphwanyikira pansi.’ ”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo taonani, kuno kulinkudza khamu la amuna, apakavalo awiriawiri. Ndipo iye anayankha nati, Babiloni wagwa, wagwa; ndi mafano onse osema a milungu yake asweka, nagwa pansi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Taonani, uyo munthu akubwera atakwera pa galeta ali ndi gulu la akavalo. Mmodzi wa iwo akuti, ‘Babuloni wagwa, wagwa! Mafano onse a milungu yake agwa pansi ndipo aphwanyika!’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo taonani, kuno kulinkudza khamu la amuna, apaakavalo awiri awiri. Ndipo iye anayankha nati, Babulo wagwa, wagwa; ndi mafano onse osema a milungu yace asweka, nagwa pansi.