Isaiah 22:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma inu mudakondwa ndi kusangalala, mudapha ng'ombe ndi nkhosa ndi kuzidya, ndiponso mudamwa vinyo. Mudati, “Tidye, timwe, poti maŵa tifa.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
koma taonani, kukondwa, ndi kusekerera, ndi kupha ng'ombe, ndi kupha nkhosa, ndi kudya nyama, ndi kumwa vinyo; tiyeni tidye ndi kumwa, chifukwa mawa tidzafa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma mʼmalo mwake inu munakondwa ndi kusangalala; munapha ngʼombe ndi nkhosa; munadya nyama ndi kumwa vinyo. Inu mumati, “Tiyeni tidye ndi kumwa pakuti mawa tifa!”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
koma taonani, kukondwa, ndi kusekerera, ndi kupha ng'ombe, ndi kupha nkhosa, ndi kudya nyama, ndi kumwa vinyo; tiyeni tidye ndi kumwa, cifukwa mawa tidzafa.