Isaiah 22:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chauta Wamphamvuzonse adandiwululira pondinong'oneza m'khutu kuti, “Ndithudi, tchimo limeneli sindidzakukhululukirani mpaka kufa kwanu,” akutero Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo Yehova wa makamu wadzivumbulutsa yekha m'makutu mwanga, Ndithu choipa chimenechi sichidzachotsedwa pa inu kufikira inu mudzafa, ati Ambuye, Yehova wa makamu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Yehova Wamphamvuzonse wandiwululira mondinongʼoneza kuti, “Tchimo limeneli sindidzakhululuka mpaka tsiku la kufa kwanu,” akutero Ambuye, Yehova Wamphamvuzonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo Yehova wa makamu wadzibvumbulutsa yekha m'makutu mwanga, Ndithu coipa cimeneci sicidzacotsedwa pa inu kufikira inu mudzafa, ati Ambuye, Yehova wa makamu.