Isaiah 22:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adzakusandutsa ngati mpira ndipo adzakuponya m'dziko lalikulu. Kumeneko nkumene ukafere, ndipo magaleta ako amene unkanyadira adzatsalira komwekonso, iwe wochititsa manyazi nyumba ya mbuye wakowe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Iye ndithu adzakuzunguza, ndi kukuponyaponya ngati mpira m'dziko lalikulu; kumeneko iwe udzafa, ndipo kumeneko kudzakhala magaleta a ulemerero wako, iwe wochititsa manyazi banja la mbuye wako.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Iye adzakukulunga kwambiri ngati mpira ndipo adzakuponyera mʼdziko lalikulu. Kumeneko ndiko ukafere ndipo kumeneko ndiko kudzatsalire magaleta ako. Ndipo udzasanduka wochititsa manyazi nyumba ya mbuye wako.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Iye ndithu adzakuzunguza, ndi kukuponyaponya ngati mpira m'dzido lalikuru; kumeneko iwe udzafa, ndipo kumeneko kudzakhala magareta a ulemerero wako, iwe wocititsa manyazi banja la mbuye wako.