Isaiah 22:25 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsiku limenelo chikhomo chokhoma dzolimba chija chidzasukusa, chidzazuka ndipo chidzagwa. Tsono zonse zopachikidwa pachikhomopo zidzaonongedwa.” Akutero Chauta Wamphamvuzonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Tsiku limenelo, ati Yehova wa makamu, chikhomo chokhomeredwa polimba udzasukusika; nudzaguluka, ndi kugwa, ndi katundu wopachikidwapo adzadulidwa; pakuti Yehova wanena.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Yehova Wamphamvuzonse akunena kuti, ‘Tsiku limeneli chikhomo chokhomedwa kwambiri chija sichidzalimbanso; chidzazuka ndipo chidzagwa ndipo zonse zopachikidwa zidzawonongedwa.’ ” Yehova wayankhula chomwechi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Tsiku limenelo, ati Yehova wa makamu, msomali wokhomeredwa polimba udzasukusika; nudzaguluka, ndi kugwa, ndi katundu wopacikidwapo adzadulidwa; pakuti Yehova wanena.