Isaiah 22:3 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atsogoleri anu onse adathaŵa nagwidwa, osaponyako ndi muvi umodzi womwe. Nonsenu amene mudapezeka mudagwidwa, ngakhale mudaathaŵiratu adani akali kutali.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Olamulira ako onse athawa pamodzi, anamangidwa ndi amauta; opezedwa ako onse anamangidwa pamodzi, nathawira patali.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Atsogoleri ako onse ngakhale anathawa limodzi; koma anagwidwa osadziteteza nʼkomwe. Inu munapezeka ndipo nonse pamodzi munatengedwa ukapolo, ngakhale munathawa pamene mdani akanali patali.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Olamulira ako onse athawa pamodzi, anamangidwa ndi amauta; opezedwa ako onse anamangidwa pamodzi, nathawira patari.