Isaiah 22:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nchifukwa chake ndidati, “Muchoke, mundileke ndilire ndi mtima woŵaŵa. Musayese kundipepesa pa za kuwonongeka kwa abale anga.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chomwecho ndinati, Usandiyang'ane ine, ndilira ndi kuwawa mtima; usafulumire kunditonthoza ine, chifukwa cha kufunkhidwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Nʼchifukwa chake Ine ndinati, “Chokani pamaso panga; ndilekeni ndilire ndi mtima wowawa. Musayesere kunditonthoza chifukwa cha kuwonongeka kwa anthu anga.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Comweco ndinati, Usandiyang'ane ine, ndilira ndi kuwawa mtima; usafulumire kunditonthoza ine, cifukwa ca kufunkhidwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga,