Isaiah 22:5 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nthaŵi ino ndi yamavuto, yogonjetsedwa ndiponso yachisokonezo m'chigwa chooneramo zinthu m'masomphenya. Ambuye, Chauta Wamphamvuzonse, ndiwo atichita zimenezi. Malinga adagumuka ndipo anthu adakalirira ku mapiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pakuti nditsiku laphokoso, ndi lopondereza pansi, ndi lothetsa nzeru, lochokera kwa Ambuye Yehova wa makamu, m'chigwa cha masomphenya, kugumuka kwa malinga, ndi kufuulira kumapiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Lero Ambuye Yehova Wamphamvuzonse walola kuti tione mavuto ndi kugonjetsedwa ndiponso chisokonezo mʼChigwa cha Masomphenya. Malinga agumuka, komanso anthu akanalira mofuwula ku mapiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pakuti ndi tsiku laphokoso, ndi lopondereza pansi, ndi lothetsa nzeru, locokera kwa Ambuye Yehova wa makamu, m'cigwa ca masomphenya, kugumuka kwa malinga, ndi kupfuulira kumapiri.