Isaiah 22:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zigwa zanu zachonde zinali zodzaza ndi magaleta, ndipo asilikali okwera pa akavalo adakaima kumaso kwa zipata za mzinda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo panali kuti zigwa zako zosankhika zinadzala magaleta, ndi apakavalo anadzinika okha pachipata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Zigwa zanu zachonde ndi zodzaza ndi magaleta, ndipo asilikali okwera pa akavalo ayikidwa pa zipata za mzinda;
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo panali kuti zigwa zako zosankhika zinadzala magareta, ndi apakavalo anadzinika okha pacipata.