Isaiah 23:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Nawu ulosi wonena za Tiro. Fuulani mwachisoni, inu oyendetsa zombo za ku Tarisisi! Pakuti mzinda wa Tiro waonongeka, kulibenso nyumba kapena dooko! Zimenezi adazimva pochokera ku Kitimu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Katundu wa Tiro. Kuwani, inu ngalawa za Tarisisi; chifukwa wapasudwa, kulibenso nyumba, kulibe polowera; kuchokera kudziko la Kitimu kwavumbulutsidwa kwa iwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Uthenga wonena za Turo: Lirani mofuwula, inu oyendetsa sitima za pa madzi za ku Tarisisi: pakuti mzinda wa Turo wawonongedwa ndipo mulibe nyumba kapena dooko. Zimenezi anazimva pochokera ku Kitimu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Katundu wa Turo. Kuwani, inu ngalawa za Tarisi; cifukwa wapasudwa, kulibenso nyumba, kulibe polowera; kucokera ku dziko la Kitimo kwabvumbulutsidwa kwa iwo.